Masalimo 92 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 92Salimo. Nyimbo ya pa tsiku la Sabata.

1Nʼkwabwino kutamanda Yehova

ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba,

2Kulengeza chikondi chanu mmawa,

ndi kukhulupirika kwanu nthawi ya usiku,

3kuyimbira nyimbo choyimbira cha zingwe khumi

ndi mayimbidwe abwino a zeze.

4Pakuti Inu mumandisangalatsa ndi ntchito zanu, Inu Yehova;

Ine ndikuyimba mwachimwemwe pa ntchito ya manja anu.

5Ndi yayikuludi ntchito yanu Yehova,

maganizo anu ndi ozamadi!

6Munthu wopanda nzeru sadziwa,

zitsiru sizizindikira,

7kuti ngakhale anthu oyipa aphuka ngati udzu

ndipo anthu onse ochita zoyipa apindula,

adzawonongedwa kwamuyaya.

8Koma Inu Yehova, ndinu wokwezedwa kwamuyaya.

9Zoonadi adani anu Yehova,

zoonadi adani anu adzawonongeka;

onse ochita zoyipa adzabalalitsidwa.

10Inu mwakweza nyanga yanga ngati nyanga ya njati;

mafuta abwino akhuthulidwa pamutu wanga.

11Maso anga aona kugonjetsedwa kwa olimbana nane,

makutu anga amva za kugwa kwa amaliwongo anga oyipa.

12Anthu olungama adzaphuka ngati mtengo wa mgwalangwa,

adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni;

13odzalidwa mʼnyumba ya Yehova,

adzakula bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu.

14Iwo adzaberekabe zipatso mu ukalamba wawo,

adzakhala anthete ndi obiriwira,

15kulengeza kuti, “Yehova ndi wolungama;

Iye ndiye Thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe choyipa.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help