Yeremiya 45 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Uthenga kwa Baruki

1Uwu ndi uthenga umene mneneri Yeremiya anawuza Baruki mwana wa Neriya mʼchaka cha chinayi cha Yehoyakimu mwana wa mwana ya Yosiya kuti alembe mʼbuku.

2“Yehova Mulungu wa Israeli, akunena kwa iwe Baruki kuti:

3Iwe unati, ‘Kalanga ine! Yehova wawonjezera chisoni pa mavuto anga. Ine ndatopa ndi kubuwula ndipo sindikupeza mpumulo.’ ”

4Koma Yehova akukuwuza kuti, “Ndidzagwetsa chimene ndinamanga ndipo ndidzazula chimene ndinadzala. Ndidzachita zimenezi mʼdziko lonse.

5Kodi tsono ukudzifunira wekha zinthu zazikulu? Usadzifunire. Pakuti ndidzagwetsa mavuto pa anthu onse, koma ndidzasunga moyo wako kulikonse kumene ungadzapite.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help