Masalimo 61 - The Word of God in Contemporary Chichewa

Salimo 61Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Loyimbidwa ndi zipangizo za zingwe.

1Imvani kulira kwanga, Inu Mulungu;

mvetserani pemphero langa.

2Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inu

ndimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka;

tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo.

3Pakuti Inu mwakhala pothawirapo panga,

nsanja yolimba polimbana ndi adani anga.

4Ine ndikulakalaka kukhala mʼtenti yanu kwamuyaya

ndi kupeza chitetezo mu mthunzi wa mapiko anu.

5Pakuti Inu Mulungu mwamva malumbiro anga;

mwandipatsa cholowa cha iwo amene amaopa dzina lanu.

6Wonjezerani masiku a moyo wa mfumu,

zaka zake kwa mibado yochuluka.

7Iye akhale pa mpando waufumu pamaso pa Mulungu kwamuyaya;

ikani chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu kuti zimuteteze.

8Kotero ndidzayimba matamando kwamuyaya pa dzina lanu

ndi kukwaniritsa malumbiro anga tsiku ndi tsiku.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help